2 Chronicles 30:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musati muumitse makosi anu monga m'mene ankachitira makolo anu, koma mudzipereke kwa Chauta, ndipo muzibwera ku Nyumba yake imene Chautayo waiyeretsa mpaka muyaya. Ndipo muzitumikira Chauta, Mulungu wanu, kuti mkwiyo wake woopsa ukuchokeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ace opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kwa inu.