2 Chronicles 30:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwatu ngati inu mubwerera kwa Chauta, anthu amene adagwira ukapolo abale anu ndi ana anu, adzachita chifundo, ndipo abale anuwo adzabweranso ku dziko lino. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi wokoma mtima ndi wachifundo, ndipo sadzakufulatirani ngati mubwerera kwa Iyeyo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,