2 Chronicles 31:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonsezi zitatha, Aisraele onse amene analipo adapita ku mizinda ya Yuda, nakaphwanyaphwanya zipilala, kugwetsa mafano, ndi kuwononga akachisi ndiponso maguwa ku dziko lonse la Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase, mpaka kuwonongeratu zonse. Pambuyo pake Aisraele onse adabwereranso kumapita kumizinda kwao, aliyense ku dziko lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumidzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efuremunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumidzi yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonse zitatha, Aisraeli onse amene anali kumeneko anapita ku mizinda ya ku Yuda, nakaphwanya miyala yachipembedzo ndi kudula mitengo ya mafano a Asera. Iwo anakawononga malo achipembedzo ndi maguwa ansembe amene anali mʼdziko lonse la Yuda, Benjamini, Efereimu ndi Manase. Atawononga zonsezi, Aisraeli anabwerera ku mizinda yawo ndi ku malo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citatha ici conse tsono, Aisrayeli onse opezekako anaturuka kumka ku midzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efraimunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israyeli anabwerera, yense ku dziko lace ndi ku midzi yao.