2 Chronicles 31:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azariya mkulu wa ansembe amene anali wa m'banja la Zadoki, adamuyankha kuti, “Chiyambire chake cha kupereka zopereka zao ku Nyumba ya Chauta, takhala ndi zinthu zambiri zakudya, ndipo zotsalanso nzambiri. Pakutitu Chauta wadalitsa anthuwo, kotero kuti tili nazo zambirimbiri zotsalazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Azariya wansembe wamkuru wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Ciyambire anthu anabwera nazo zopereka ku nyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zatitsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ace; ndipo suku kucuruka kwa cotsala.