2 Chronicles 31:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adabwera nazo zoperekazo mokhulupirika, zigawo zachikhumi ndiponso zinthu zopatulika. Tsono kapitao wamkulu woŵayang'anira anali Konaniya Mlevi, pamodzi ndi Simei mbale wake, amene anali wachiŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkuru woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wace ndiye wotsatana naye.