2 Chronicles 31:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Kore, mwana wa Imina Mlevi, amene ankalonda pa chipata chakuvuma ndiye ankayang'anira nsembe zaulere zopereka kwa Mulungu. Ankapatula chigawo cha zopereka choyenera Chauta ndiponso zopereka zoyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Kore mwana wa Imna Mlevi, wa ku cipata ca kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulikitsa.