2 Chronicles 31:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, ndiwo amene ankamthandiza mokhulupirika ku mizinda ya ansembe, popereka magawo a zopereka kwa abale ao, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, molingana ndi magulu ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Miniyamini, ndi Yesuwa, ndi Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akulu monga ang'ono;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Minyamini, ndi Yesuwa; ndi Semaya, Amariya, ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akuru monga ang'ono;