2 Chronicles 31:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komanso ankapereka kwa anthu olembedwa potsata mabanja a anthu, ndiye kuti amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka kupitirirapo, amene ankaloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti azigwira ntchito yofunika pa tsiku lake, malinga ndi nthaŵi yao ndi magulu ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera apa, amagawira ana aamuna a zaka zitatu kapena kupitirira amene mayina awo anali mʼmbiri ya mibado yawo, amene adzalowe mʼNyumba ya Yehova kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku za magulu awo, molingana ndi udindo ndi magulu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa ali yense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa nchito yace pa tsiku lace, kukacita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;