2 Chronicles 31:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe ankaŵalemba potsata mabanja a makolo ao. Alevi ankaŵalemba kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mtundu wa ntchito yao ndi magulu ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;