2 Chronicles 31:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za ansembe, ana a Aaroni amene ankakhala ku madera okhala ndi mabusa a mizinda yao, panali amuna ena m'mizinda yoŵerengeka, amene adaauzidwa pakuŵatchula maina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pa ansembewo, ndiponso kwa aliyense pakati pa Alevi amene adalembedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za ansembe, zidzukulu za Aaroni, amene amakhala mʼminda yozungulira mizinda yawo kapena mzinda wina uliwonse, anthu anasankhidwa mowatchula mayina kuti azipereka magawo kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pawo ndiponso kwa onse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado ya Alevi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uli wonse, ochulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa cibadwidwe magawo ao.