2 Chronicles 31:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adakhazikitsanso magulu a ansembe ndi a Alevi, gulu lililonse kutsata ntchito yake. Ansembe ndi Aleviwo ena adaŵaika kuti azipereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, ena kumatumikira ku zipata za bwalo la Chauta, ena kumathokoza ndi kutamanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wace, ndi ansembe ndi Alevi, acite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, ku zipata za cigono ca Ambuye.