2 Chronicles 31:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito iliyonse imene ankachita potumikira ku Nyumba ya Chauta potsata malangizo ndi malamulo, ndi pofunafuna Mulungu wake, ankachita zimenezo ndi mtima wake wonse ndipo ankapeza mwai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa chilichonse chimene anachita pa ntchito ya Nyumba ya Mulungu ndi pa kumvera malangizo ndi malamulo, iye anafunafuna Mulungu wake ndipo anagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Ndipo zinthu zimamuyendera bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'nchito iri yonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'cilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wace, anacita ndi mtima wace wonse, nalemerera nayo.