2 Chronicles 31:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idapatula chigawo cha chuma chake, kuti zipezeke nsembe zopsereza izi: zam'maŵa, zamadzulo, za masiku a Sabata, za pachiyambi pa mwezi ndiponso za masiku a chikondwerero okhazikitsidwa, monga momwe zidalembedwera m'malamulo a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera pa chuma chake, mfumu inapereka nsembe zopsereza za mmawa ndi madzulo ndiponso nsembe zopsereza za pa Chikondwerero cha Masabata, Chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndipo inakhazikitsa zikondwerero monga zinalembedwera mʼmalamulo a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naikanso gawo la mfumu lotapa pa cuma cace la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova.