2 Chronicles 31:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono lamulo limenelo atangolilengeza, pomwepo Aisraele adayamba kupereka kwambiri zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pobuka mau aja, ana a Israyeli anapereka mocuruka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uci, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mocuruka.