2 Chronicles 31:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ndi Ayuda amene ankakhala ku mizinda ya Yuda, ankabwera ndi zigawo zachikhumi za ng'ombe ndi nkhosa, ndiponso zinthu zopatulika zimene anali atazipereka kwa Chauta, Mulungu wao, namaziika zonsezo m'milum'milu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana a Israyeli ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyuru miyuru,