2 Chronicles 31:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hezekiya ndi nduna zake atabwera naona miluyo, adatamanda Chauta pamodzi ndi Aisraele anthu ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Hezekiya ndi akuru ace anadza, naona miyuruyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ace Aisrayeli.