2 Chronicles 32:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake, zitatha ntchito zachikhulupirirozi, Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adabwera kudzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo adamanga zithando zankhondo kuzinga mizinda yamalinga. Ankati aŵagumule malinga akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha zonse zimene Hezekiya anachita mokhulupirika, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kuthira nkhondo dziko la Yuda. Iye anazinga mizinda yotetezedwa ya Yuda, kuganiza kuti ayigonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Sanakeribu mfumu ya Asuri, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.