2 Chronicles 32:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi si Hezekiya yemweyu amene adachotsa akachisi ndi maguwa ku mapiri, nalamula anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu kuti, “Muzipembedza ku guwa limodzi lokha ndipo muzipereka nsembe zanu zopsereza pa guwa limodzi lokhalo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi si Hezekiya amene anachotsa malo opembedzerapo Mulungu ameneyu ndi maguwa ansembe ndi kunena kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe limodzi ndi kupserezapo nsembe?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sanaicotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire ku guwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?