2 Chronicles 32:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi inu simukudziŵa zimene ine ndi makolo anga takhala tikuichita mitundu yonse ya anthu a maiko ena? Kodi milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maikowo idatha kupulumutsa maiko ao m'manja mwanga?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi inu simukudziwa zimene ine ndi makolo anga tachita kwa anthu a mitundu ina? Kodi milungu ya mitundu imeneyi inatha kupulumutsa dziko lawo kuchoka mʼdzanja langa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simudziwa kodi comwe ine ndi makolo anga tacitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?