2 Chronicles 32:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi pakati pa milungu ya mitundu ina ya anthuyo, imene makolo anga adaiwononga kotheratu, ndi uti amene adatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga, kuti inuyo muziti Mulungu wanu adzakupulumutsani m'manja mwanga?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndi milungu iti mwa milungu ya mitundu ina ya anthuwo, imene makolo anga anayiwononga kotheratu, inatha kupulumutsa anthu ake mʼdzanja langa? Nanga tsono Mulungu wanuyo adzakupulumutsani mʼdzanja langa motani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga, kuti Mulungu wako adzakhoza kukulanditsa iwe m'dzanja mwanga?