2 Chronicles 32:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye inutu tsono, musalole kuti Hezekiya akunyengeni kapena kukusokezani motero ai, ndipo musamkhulupirire. Chifukwa palibe mulungu wa mtundu kapena ufumu wina uliwonse amene adatha kuŵapulumutsa anthu ake m'manja mwanga kapena m'manja mwa makolo anga. Mulungu wanuyo sadzatha kukupulumutsani m'manja mwanga ai.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho inu musalole kuti Hezekiya akunamizeni ndi kukusocheretsani motere. Musamukhulupirire, pakuti palibe mulungu wa mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse umene unatha kupulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa kapena mʼdzanja la makolo anga. Nanga bwanji Mulungu wanuyo, sadzatha kukupulumutsani kuchoka mʼdzanja langa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe mulungu wa mtundu uli wonse wa anthu, kapena ufumu uli wonse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?