2 Chronicles 32:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Senakeribu adalemba makalata achipongwe oputa Chauta, Mulungu wa Aisraele, adati, “Monga milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maiko ena sidathe kuŵapulumutsa anthu ao m'manja mwanga, momwemonso Mulungu wa Hezekiya sadzatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m'dzanja mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumunso inalemba makalata onyoza Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo inanena zotsutsana naye izi: “Monga momwe milungu ya anthu a mayiko ena sinathe kuwapulumutsa kuchoka mʼdzanja langa, chonchonso Mulungu wa Hezekiya sadzapulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ace m'dzanja mwanga.