2 Chronicles 32:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthuwo mofuula adalengeza zimenezi m'chilankhulo cha Chiyuda kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuti aŵachititse mantha ndi kuŵaopsa, ndi cholinga choti alande mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafuula ndi mau akulu m'chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mudziwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iwo anafuwula mu Chihebri kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuwaopseza ndi kuwachititsa mantha ndi cholinga choti alande mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapfuula ndi mau akuru m'cinenedwe ca Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwabvuta, kuti alande mudziwu.