2 Chronicles 32:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adatuma mngelo, ndipo iye adadzapha ankhondo onse amphamvu, atsogoleri ndi akulu a ku zithando za mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu adabwerera kumapita ku dziko la kwao ali ndi nkhope yamanyazi. Ndipo atakaloŵa m'nyumba ya Chauta wake, ana ake ena adamupha momwemo ndi lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anatumiza mngelo amene anadzapha anthu onse odziwa nkhondo ndi atsogoleri ndiponso oyangʼanira misasa ya mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu anabwerera kwawo wamanyazi. Ndipo atalowa mʼnyumba ya mulungu wake, ena mwa ana ake anamupha ndi lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, ku cigono ca mfumu ya Asuri. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi ku dziko lace. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wace, iwo oturuka m'matumbo mwace anamupha ndi lupanga pomwepo.