2 Chronicles 32:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu ambiri adabwera ndi zopereka kwa Chauta ku Yerusalemu, nadzaperekanso mphatso kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda. Zitachitika zimenezo, Hezekiyayo adakhala wolemekezeka kwambiri pamaso pa mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wace, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.