2 Chronicles 32:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Hezekiya sadachite molingana ndi zabwino zimene Chauta adaamchitira, poti mtima wake unali wodzitama. Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta udamugwera iyeyo, ndiponso anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Hezekiya anali ndi mtima wonyada ndipo sanachite molingana ndi kukoma mtima kumene Mulungu anamuonetsera. Choncho mkwiyo wa Yehova unali pa iye ndi pa Yuda ndi Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.