2 Chronicles 32:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kenaka Hezekiya adadzichepetsa naleka kudzikuza, iyeyo ndi anthu amene ankakhala mu Yerusalemu. Motero mkwiyo wa Chauta sudagwe pa anthuwo pa masiku a Hezekiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Hezekiya anadzichepetsa m'kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kenaka Hezekiya analapa za kunyada kwakeko, monga anachitanso anthu a mu Yerusalemu. Choncho mkwiyo wa Yehova sunafike pa iwo pa nthawi ya Hezekiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.