2 Chronicles 32:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya anali wolemera kwambiri ndiponso waulemu zedi. Tsono adadzimangira nyumba zomasungiramo chuma cha siliva, golide, miyala yamtengowapatali, zonunkhira, zishango ndiponso mitundu yonse ya ziŵiya zamtengowapatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cuma ndi ulemu zinacurukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golidi, ndi timiyala ta mtengo wace, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma ziri zonse;