2 Chronicles 32:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiyayu ndiye amene adaatseka ngalande yakumtunda ya madzi a ku Gihoni, nkuŵaongolera kuti atsikire kuzambwe kwa mzinda wa Davide. Ankakhoza pa ntchito zonse zimene ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi Hezekiya amene anatseka ku mtunda kwa kasupe wa Gihoni, ndi kumuwongolera kuti madzi ake apite mbali ya kumadzulo kwa Mzinda wa Davide. Iye ankachita bwino pa ntchito iliyonse imene ankagwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire ku madzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo nchito zace zonse.