2 Chronicles 32:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho pamene amithenga a nduna za ku Babiloni adatumidwa kwa Hezekiya kuti akafunse za chizindikiro chija chimene chidachitika m'dzikomo, Mulungu adamsiya yekha, kuti amuyese ndipo kuti adziŵe zonse za mumtima mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene nthumwi zotumizidwa ndi atsogoleri a ku Babuloni zinabwera kudzamufunsa za chizindikiro chozizwitsa chimene chinachitika mʼdzikomo, Mulungu anamusiya yekha, kumuyesa kuti adziwe zonse zimene zinali mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babulo, amene anatumiza kwa iye kufunsira za codabwiza cija cidacitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwace.