2 Chronicles 32:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adamwalira, naikidwa ku chikwera ku manda a ana a Davide. Anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi a mu Yerusalemu adamchitira ulemu pa maliro ake. Tsono Manase mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pa phiri pamene pali manda a zidzukulu za Davide. Ayuda onse ndi anthu a mu Yerusalemu anamulemekeza atamwalira. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ace, namuika polowerera ku manda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamcitira ulemu pa imfa yace. Ndipo Manase mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.