2 Chronicles 32:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo anthu ambiri adasonkhana kuti atseke akasupe onse pamodzi ndi mfuleni womwe umene unkayenda m'kati mwa nthakamo. Iwo ankati, “Akafika kuno mafumu a ku Asiriya, adzapezerenji madzi ambiri?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu lalikulu la anthu linasonkhana, ndipo anatseka akasupe onse pamodzi ndi mtsinje umene umayenda mʼkati mwa nthakamo. Iwo ankanena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mafumu a Asiriya akabwera kuno adzapeze madzi ambiri?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asuri ndi kupeza madzi ambiri.