2 Chronicles 32:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adalimba mtima, nayamba kumanganso khoma limene linali litagamuka. Tsono adamanganso nsanja pakhomapo, ndiponso ina kunja kwake. Adalimbitsanso linga lotchedwa Milo ku mzinda wa Davide. Adapanga zida zankhondo ndi zishango zambirimbiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye anagwira ntchito molimbika kukonza madera ogumuka a khoma ndi kumangapo msanja. Anamanganso mpanda wina kunja kwa mpanda winawo ndipo anamanga zolimbitsa Milo ku mzinda wa Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwace, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zocuruka.