2 Chronicles 32:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo ali ndi gulu lankhondo la anthu, koma ife tili ndi Chauta, Mulungu wathu, wotithandiza ndi wotimenyera nkhondo zathu.” Apo anthuwo adakhulupirira mau a Hezekiya mfumu ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ali ndi mphamvu ya anthu basi, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kutithandiza ndi kuchita nkhondo zathu.” Ndipo anthu anapeza chilimbikitso kuchokera pa zimene Hezekiya mfumu ya Yuda ananena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anacirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.