2 Chronicles 32:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pa zimenezi Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, amene anali atazinga mzinda wa Lakisi pamodzi ndi ankhondo ake onse, adatuma akazembe ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi kwa anthu onse a ku Yuda amene anali mu Yerusalemu. Adaŵatuma ndi mau akuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ina, pamene Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo anali atazinga Lakisi, iye anatumiza atsogoleri ake ankhondo ku Yerusalemu ndi uthenga uwu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a ku Yuda amene anali kumeneko:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambuyo pace Sanakeribu mfumu ya Asuri, akali ku Lakisi ndi mphamvu yace yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,