2 Chronicles 33:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye pamene anali pa mavuto, adapempha kuti Chauta, Mulungu wake, amkomere mtima, ndipo adadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wace, nadzicepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ace.