2 Chronicles 33:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adamanga khoma la kunja kwa mzinda wa Davide kuzambwe kwake kwa Gihoni, kuchokera ku chigwa mpaka poloŵera ku Chipata cha Nsomba. Ndipo adamanga khomalo kuzungulira Ofele nalikweza kwambiri. Adaikanso atsogoleri ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitatha ichi tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa chipata chansomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitapita izi iye anamanga khoma la kunja kwa Mzinda wa Davide kumadzulo kwa kasupe wa Gihoni ku chigwa mpaka polowera ku Chipata cha Nsomba kuzungulira phiri la Ofeli. Iyeyo anakweza kwambiri khomalo. Anayikanso atsogoleri a nkhondo ku mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citatha ici tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'cigwa, mpaka polowera pa cipata cansomba; nazinga Ofeli, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.