2 Chronicles 33:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachotsa milungu yachilendo ndiponso fano m'Nyumba ya Mulungu. Adachotsa maguwa onse achikunja amene anali ataŵamanga pa phiri la Chauta ku Yerusalemu. Ndipo adaŵataya kunja kwa mzinda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachotsa milungu yonse yachilendo ndi fano mʼNyumba ya Yehova komanso maguwa ansembe onse amene anamanga pa phiri la Nyumba ya Mulungu ndi mu Yerusalemu, nazitayira kunja kwa mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.