2 Chronicles 33:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanganso guwa la Chauta, namaperekerapo nsembe zachiyanjano ndiponso nsembe zothokozera. Tsono adalamula anthu a ku Yuda kuti azitumikira Chauta Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anabwezeretsa guwa lansembe la Yehova ndi kupereka zopereka zachiyanjano ndiponso zopereka zamatamando ndipo anawuza Yuda kuti atumikire Yehova Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israyeli.