2 Chronicles 33:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina zonse za Manase, pamodzi ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndiponso mau a aneneri amene adalankhula naye m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mafumu a ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m'machitidwe a mafumu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Manase, kuphatikiza mapemphero ake kwa Mulungu wake ndi mawu amene alosi anayankhula kwa iye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli, zalembedwa mʼmabuku a mafumu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lace kwa Mulungu wace, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli, taonani, zalembedwa m'niacitidwe a mafumu a Israyeli.