2 Chronicles 33:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'nyumba mwake. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manase anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yake yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Manase anagona ndi makolo ace, namuika m'nyumba mwace mwace; ndi Amoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.