2 Chronicles 33:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadadzichepetse pamaso pa Chauta monga momwe Manase bambo wake adadzichepetsera. Koma Amoniyu ankadzipereka ku machimo kosalekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sanadzicepetsa pamaso pa Yehova, monga umo anadzicepetsera Manase atate wace; koma Amoni amene anacurukitsa kuparamula kwace.