2 Chronicles 33:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu Amoniyo. Kenaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anakonzera chiwembu mfumu Amoni, ndipo anayika mwana wake Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira ciwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wace akhale mfumu m'malo mwace.