2 Chronicles 33:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapititsanso ana ace pamoto m'cigwa ca ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.