2 Chronicles 33:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'Nyumba ya Chauta adaikamo fano lopanga iyeyo, Nyumba imene Mulungu adaauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba imeneyi, mu Yerusalemu muno, malo amene ndaŵasankhula pakati pa mafuko onse a Aisraele, ndimo m'mene adzatamandira dzina langa mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika cifanizo cosema ca fanolo adacipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomo mwana wace, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israyeli ndidzaika dzina langa ku nthawi zonse;