2 Chronicles 34:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adapereka ndalamazo kwa akapitao oyang'anira Nyumba ya Chauta. Adaperekako ndalama zina kwa anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Chauta, kuti aikonze ndi kuilimbitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anazipereka m'dzanja la anchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa anchito akucita m'nyumba ya Yehova, kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;