2 Chronicles 34:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaperekanso ndalama zina kwa amisiri amatabwa ndi kwa amisiri omanga nyumba, kuti agule miyala yosema ndi mitengo ya mitanda ndi phaso la nyumba, zimene mafumu a ku Yuda adaalola kuti ziwonongeke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.