2 Chronicles 34:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imene ankatulutsa ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta, wansembe Hilikiya adapeza buku la Malamulo a Chauta, Malamulo aja amene Mulungu adaaŵapereka kudzera mwa Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakutulutsa ndalama zimene adalowa nazo kunyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imene ankatulutsa ndalama zimene anabwera nazo ku Nyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya anapeza Buku la Malamulo limene linaperekedwa kudzera mwa Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuturutsa ndarama zimene adalowa nazo ku nyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la cilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.