2 Chronicles 34:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pitani, mukafunse kwa Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu otsala ku Israele ndi ku Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a Chauta, sadatsate zonse zimene zalembedwa m'bukuli.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israele ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukulu; popeza makolo athu sanasunge mau a Yehova kuchita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israyeli ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukuru; popeza makolo athu sanasunga mau a Yehova kucita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.