2 Chronicles 34:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Hilikiya, pamodzi ndi anthu amene mfumu idaŵatuma aja, adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu, anali mwana wa Tokati, mwana wa Hasira. Mkaziyo ankakhala ku Yerusalemu m'dera lachiŵiri la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye adamuuza za nkhaniyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hilikiya pamodzi ndi anthu amene anawatuma aja, anapita kukayankhula ndi mneneri wamkazi Hulida, amene anali mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira, wosunga zovala zaufumu. Hulida ankakhala mu Yerusalemu, mʼdera lachiwiri la mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasire wosunga zobvala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nanena naye mwakuti.